< Yesaya 60 >
1 “Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika, ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
2 Taona, mdima waphimba dziko lapansi ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina, koma Yehova adzakuwalira iwe, ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.
4 “Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika. Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe; ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
5 Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri, mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe; chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
6 Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako, ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai. Ndipo onse a ku Seba adzabwera atanyamula golide ndi lubani uku akutamanda Yehova.
7 Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu, nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani; zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe, ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
8 “Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo, ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?
9 Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali; patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi, zikubweretsa ana ako ochokera kutali, pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo, kudzalemekeza Yehova Mulungu wako, Woyerayo wa Israeli, pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
10 “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu awo adzakutumikira. Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo.
11 Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse, sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku, kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo, akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
12 Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe; adzawonongeka kotheratu.
13 “Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini, mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanoni kuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika; ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
14 Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani; onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu. Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova; Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
15 “Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe, koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe cha anthu amibado yonse.
16 Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthu ndi kuleredwa pa maere aufumu, motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako, Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo.
17 Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa, ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo. Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala. Olamulira ako adzakhala a mtendere. Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
18 Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako, bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako, ndidzakhala malinga ako okuteteza ndipo udzanditamanda.
19 Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire, kapena mwezi kuti uwunikire usiku, pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya, ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
20 Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzazimiriranso; Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya, ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
21 Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya. Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala, ntchito ya manja anga, kuti aonetse ulemerero wanga.
22 Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko, kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu. Ine ndine Yehova, nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”