< Machitidwe a Atumwi 9 >

1 Pa nthawi imeneyi, Saulo ankaopsezabe okhulupirira Ambuye nafuna kuwapha. Iye anapita kwa mkulu wa ansembe,
Saul se však snažil Ježíšovy následovníky zastrašit a zlikvidovat.
2 ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu.
Vyžádal si od velekněze pověřující listiny pro židovské synagogy v Damašku. Chtěl tam pátrat po křesťanech, mužích i ženách, zatknout je a přivést do Jeruzaléma před soud.
3 Akuyandikira ku Damasikoku paulendo wake, mwadzidzidzi kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira iye.
Vydal se tam se svým doprovodem a byl již před branami Damašku, když ho obklopilo zvláštní světlo z nebe.
4 Iye anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti, “Saulo, Saulo ukundizunziranji Ine?”
V úleku padl na zem a uslyšel hlas: „Saule, Saule, proč mne pronásleduješ?“
5 Saulo anafunsa kuti, “Ndinu yani Ambuye?” Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza.”
Zeptal se: „Ale kdo jsi, pane?“Pán mu odpověděl: „Já jsem Ježíš a ty mne pronásleduješ v mých učednících. Je to stejné, jako bys chtěl hlavou rozbít zeď.“Saul zlomený hrůzou řekl: „Pane, čekám na tvoje rozkazy.“
6 “Tsopano dzuka, lowa mu mzindamo, ndipo udzawuzidwa zoyenera kuchita.”
A Pán k němu: „Vstaň, jdi do města a tam se dozvíš další.“
7 Anthu amene anali naye paulendo, anasowa chonena; iwo anamva mawu koma sanaone wina aliyense.
Muži ze Saulova doprovodu stáli v úžasu; něco slyšeli, ale nevěděli, s kým jejich velitel mluví.
8 Saulo anayimirira, ndipo pamene anatsekula maso ake sanathe kuona. Kotero anamugwira dzanja ndi kulowa naye mu Damasiko.
Saul se zvedl ze země, protíral si oči, ale neviděl nic; oslepl. Uchopili ho za ruce, a tak ho odvedli do Damašku.
9 Anakhala wosaona kwa masiku atatu ndiponso sanadye kapena kumwa kanthu kalikonse.
Tři dny trvala jeho slepota a po celou tu dobu nic nejedl ani nepil.
10 Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya. Ambuye anamuyitana mʼmasomphenya kuti, “Hananiya!” Iye anayankha kuti, “Ine Ambuye.”
V Damašku žil věřící muž jménem Ananiáš. Tomu se zjevil Pán Ježíš a oslovil ho jménem. Ananiáš se zeptal: „Pane, co si přeješ?“
11 Ambuye anamuwuza iye kuti, “Nyamuka, pita ku nyumba ya Yudasi imene ili pa Njira Yolunjika ndipo ukafunse za munthu wochokera ku Tarisisi dzina lake Saulo, pakuti akupemphera.
Pán mu řekl: „Vstaň a jdi do Přímé ulice. Tam v Judově domě najdeš Saula, který pochází z Tarsu.
12 Ndipo waona mʼmasomphenya munthu, dzina lake Hananiya atabwera ndi kumusanjika manja kuti aonenso.”
Při modlitbě tě uviděl, jak k němu jdeš, kladeš na něj ruce a on znovu dostává zrak. Zjevil jsem mu i tvoje jméno.“
13 Hananiya anayankha kuti, “Ambuye, ndinamva zambiri za munthu uyu ndi zonse zoyipa anachitira oyera mtima a ku Yerusalemu.
Ale Ananiáš namítl: „Pane, o tom muži kdekdo vypráví, jak mnoho zla způsobil mezi tvými věrnými v Jeruzalémě.
14 Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu ansembe kuti adzamange onse amene amayitana pa dzina lanu.”
I sem prý přišel s pověřením předních kněží, aby pozatýkal všechny, kdo vyznávají tvoje jméno.“
15 Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli.
Pán mu však řekl: „Přesto jdi. Já jsem si ho vybral za svůj zvláštní nástroj, který bude šířit zvuk mého jména nejen mezi židy, ale i mezi pohany a donese ho až před panovníky.
16 Ine ndidzamuonetsa zowawa zonse zimene ayenera kumva chifukwa cha dzina langa.”
A ukáži mu, že pro moje jméno hodně vytrpí.“
17 Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.”
Ananiáš šel a v určeném domě nalezl Saula. Položil na něj ruce a řekl: „Saule, bratře, posílá mě k tobě Pán Ježíš, který se ti ukázal na cestě k nám. Máš zase prohlédnout a být naplněn svatým Duchem.“
18 Nthawi yomweyo mʼmaso mwa Saulo munachoka zinthu zokhala ngati mamba ansomba, ndipo anayambanso kuona. Iye anayimirira nabatizidwa,
A tu jako by se protrhla tma a Saul okamžitě prohlédl. Povstal a dal se pokřtít.
19 ndipo atadya chakudya, anapezanso mphamvu. Saulo anakhala masiku angapo ndi ophunzira a ku Damasiko.
Potom se posilnil jídlem. Připojil se k damašským následovníkům Krista a byl s nimi několik dní.
20 Posakhalitsa anayamba kulalikira mʼsunagoge kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu.
Brzy však začal chodit také do synagog a veřejně hlásal, že Ježíš je Boží Syn.
21 Onse amene anamva iye akulalikira anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene anayambitsa kuzunza okhulupirira ku mpingo wa ku Yerusalemu? Kodi siwabwera kuno kuti awamange ndi kuwapereka kwa akulu a ansembe?”
Všichni posluchači se divili a říkali: „Cožpak to není ten, kdo tak tvrdě v Jeruzalémě pronásledoval Ježíšovy vyznavače? I sem přece přišel, aby je pochytal a předvedl před veleradu.“
22 Koma mphamvu za Saulo zinali kukulirakulira ndipo anathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko powatsimikizira kuti Yesu ndi Mpulumutsi.
Avšak Saula tím neumlčeli. Naopak on umlčoval damašské židy a dokazoval jim, že Ježíš je Mesiáš.
23 Patapita masiku ambiri, Ayuda anapangana zoti aphe Saulo,
Když už to trvalo dlouho, domluvili se někteří z nich, že ho zabijí.
24 koma iye anadziwa za chiwembucho. Anthu ankadikirira usana ndi usiku pa zipata za mzindawo kuti amuphe.
Saul se dozvěděl o těch úkladech, ale oni dali hlídat ve dne i v noci městské brány, aby jim neunikl.
25 Koma ophunzira ake anamutenga usiku, namutsitsira kunja kwa mpandawo mʼdengu.
Tak ho křesťané nakonec spustili v koši přes hradby.
26 Saulo atafika ku Yerusalemu, anayesetsa kulowa mʼgulu la ophunzira koma onse anamuopa chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunziradi.
Saul přišel zpět do Jeruzaléma a pokoušel se připojit k Ježíšovým následovníkům, ale všichni se ho báli; nevěřili, že by se mohl tak změnit.
27 Koma Barnaba anamutenga napita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozera iwo za mmene Saulo anaonera Ambuye pa njira paja, ndi kuti Ambuye anamuyankhula, ndi momwe analalikira ku Damasiko mʼdzina la Yesu mosaopa.
Tu se ho ujal Barnabáš, přivedl ho k apoštolům a všechno jim vyprávěl: Jak se Pán na cestě ukázal Saulovi a mluvil s ním a jak potom Saul v Damašku bez bázně hlásal Ježíše.
28 Kotero Saulo anakhala nawo nayendayenda mwaufulu mu Yerusalemu akulalikira molimba mtima mʼdzina la Ambuye.
A tak ho věřící v Jeruzalémě přijali mezi sebe a také zde směle mluvil o Pánu Ježíši.
29 Anayankhula ndi kutsutsana ndi Ayuda a Chihelene, koma iwo ankafuna kumupha.
Zvláště rád diskutoval s řecky mluvícími židy. Ti mu nakonec také ukládali o život.
30 Abale atadziwa zimenezi, anamutenga Saulo ndi kupita naye ku Kaisareya, ndipo anamutumiza ku Tarisisi.
Když se to dozvěděli bratři, odvedli ho tajně do Césareje a odtud ho poslali do rodného Tarsu.
31 Pamenepo mpingo wa ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unakhala pamtendere, unalimbikitsidwa; ndi kupatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera, unakula mʼchiwerengero, ndi kukhala moopa Ambuye.
Saulovým obrácením nastala pro sbory v Judsku, Galileji i v Samařsku pokojná doba vnitřního budování a života v oddanosti Bohu. Duch svatý mezi nimi působil, takže rostly i počtem.
32 Pamene Petro amayendera mpingo, anapita kukachezera oyera mtima a ku Luda.
Petr podnikl okružní cestu po všech sborech a přišel tak i k věřícím v Lyddě.
33 Kumeneko anakapeza munthu dzina lake Eneya, wofa ziwalo amene anagona pa mphasa kwa zaka zisanu ndi zitatu.
Navštívil tam jakéhosi Eneáše, který byl už osm let ochrnutý upoután na lůžko.
34 Petro anati kwa iye, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa iwe, dzuka ndipo yalula mphasa yako.” Nthawi yomweyo Eneya anayimirira.
Petr mu řekl: „Eneáši, Ježíš Kristus tě uzdravuje. Vstaň a skliď si své lůžko!“A on hned vstal.
35 Anthu onse amene anakhala ku Luda ndi ku Sharoni anamuona ndipo anatembenukira kwa Ambuye.
Když to viděli obyvatelé Lyddy a Sáronu, uvěřili v Pána Ježíše.
36 Ku Yopa kunali wophunzira wina dzina lake Tabita (mʼChigriki amati Dorika) amene nthawi zonse ankachita zachifundo ndiponso kuthandiza osauka.
Nedaleko Lyddy, v Joppe, žila věřící žena jménem Tabita, řecky Dorkas. Byla známá tím, jak z lásky podporovala chudé.
37 Nthawi imeneyi anadwala ndipo anamwalira, anasambitsa thupi lake, namugoneka mʼchipinda chammwamba.
Právě v těch dnech však onemocněla a zemřela. Připravili ji k pohřbu a zatím uložili do místnosti v patře.
38 Popeza ku Yopa kunali pafupi ndi Luda; pamene ophunzira anamva kuti Petro anali ku Luda, anatuma anthu awiri kuti akamudandaulire kuti, “Chonde bwerani kuno msanga!”
Věřící se doslechli, že Petr je v Lyddě, a poslali k němu s prosbou, aby k nim hned přišel.
39 Petro ananyamuka, napita nawo, ndipo atafika anamutengera ku chipinda chammwamba. Amasiye onse anayima momuzungulira akulira ndi kumuonetsa mwinjiro ndi zovala zina zimene Dorika ankapanga akanali moyo.
Petr šel s posly a ti ho vedli přímo nahoru do domu. Tam byl zástup plačících vdov, ty ho obklopily a ukazovaly mu šaty, které jim ušila jejich milá Dorkas.
40 Petro anatulutsa anthu onse mʼchipindamo; ndipo anagwada pansi ndi kupemphera. Anatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka,” Tabita anatsekula maso ake, ndipo ataona Petro anakhala pansi.
Petr požádal, aby všichni odešli, poklekl a modlil se. Po chvíli se obrátil k mrtvému tělu a řekl: „Tabito, vstaň!“Ona otevřela oči, uviděla Petra a posadila se.
41 Petro anamugwira dzanja, namuyimiritsa. Ndipo anayitana okhulupirira ndi amasiye namupereka wamoyo.
Petr jí podal ruku a pomohl jí vstát. Pak zase zavolal všechny nahoru a odevzdal jim Tabitu živou.
42 Zimenezi zinadziwika ku Yopa konse, ndipo anthu ambiri anakhulupirira Ambuye.
To se rychle rozkřiklo po celém Joppe a mnoho lidí uvěřilo v Pána Ježíše.
43 Petro anakhala ku Yopa kwa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.
Petr pak bydlel dlouho v Joppe v domě koželuha Šimona.

< Machitidwe a Atumwi 9 >