< 2 Mbiri 29 >
1 Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya.
2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide abambo ake.
3 Pa chaka choyamba cha ulamuliro wake, iye anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anazikonza.
4 Iye analowetsamo ansembe ndi Alevi ndipo anawasonkhanitsa ku bwalo lakummawa
5 ndipo anati: “Mverani, inu Alevi! Dziyeretseni tsopano ndiponso muyeretse Nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse zodetsa zonse ku malo opatulika.
6 Makolo athu anali osakhulupirika ndipo anachita zoyipa pa maso pa Yehova Mulungu wathu ndi kumusiya Yehovayo. Iwo anatembenuka ndi kusiya malo okhalako Yehova ndi kumufulatira.
7 Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli.
8 Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino.
9 Ichi nʼchifukwa chake makolo athu anaperekedwa ku lupanga ndipo nʼchifukwa chake ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo.
10 Tsono ine ndikuganiza zochita pangano ndi Yehova Mulungu wa Israeli, kuti mkwiyo wake woopsawu utichokere.
11 Ana anga, musanyalanyaze tsopano, pakuti Yehova wakusankhani kuti muziyima pamaso pake ndi kumutumikira Iye, kugwira ntchito pamaso pake ndi kufukiza lubani.”
12 Ndipo Alevi awa anakonzeka kugwira ntchito: Kuchokera ku banja la Kohati, Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya; kuchokera ku banja la Merari, Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli; kuchokera ku banja la Geresoni, Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa;
13 kuchokera kwa zidzukulu za Elizafani, Simiri ndi Yeiyeli; kuchokera kwa zidzukulu za Asafu, Zekariya ndi Mataniya;
14 kuchokera kwa zidzukulu za Hemani, Yehieli ndi Simei; kuchokera kwa zidzukulu za Yedutuni, Semaya ndi Uzieli.
15 Atasonkhanitsa abale awo ndi kudziyeretsa, iwo anapita kukayeretsa Nyumba ya Yehova, monga inalamulira mfumu, potsatira mawu a Yehova.
16 Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni.
17 Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.
18 Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse.
19 Takonza ndi kuyeretsa zinthu zonse zimene mfumu Ahazi anazichotsa mwa kusakhulupirika kwake pamene anali mfumu. Taziyika kutsogolo kwa guwa la Yehova.”
20 Mmamawa tsiku linalo, mfumu Hezekiya inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu a mu mzindawo ndipo inapita ku Nyumba ya Yehova.
21 Iwo anabweretsa ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ziwiri monga nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo la ufumu, la malo opatulika ndi Yuda. Tsono mfumu inalamula ansembe, zidzukulu za Aaroni, kuti apereke zimenezi pa guwa lansembe la Yehova.
22 Choncho anthuwo anapha ngʼombe zazimunazo ndipo ansembe anatenga magazi ake ndi kuwawaza pa guwa lansembe, kenaka anapha nkhosa zazimuna zija ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe; anaphanso ana ankhosa aja ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe.
23 Mbuzi zoperekedwa chifukwa cha tchimo zija zinabweretsedwa pamaso pa mfumu ndi anthu onse, ndipo anasanjika manja awo pa izo.
24 Kenaka ansembe anapha mbuzizo ndipo anapereka magazi ake pa guwa, kuti ukhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraeli onse, pakuti mfumu inalamula kuti nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo zichitike chifukwa cha Aisraeli onse.
25 Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri.
26 Kotero Alevi anayima okonzekera atanyamula zoyimbira za Davide ndiponso ansembe atanyamula malipenga awo.
27 Hezekiya analamulira kuti apereke nsembe zopsereza pa guwa. Pamene amayamba kupereka nsembezo, kuyimbira Yehova kunayambikanso, pamodzi ndi malipenga ndi zipangizo zoyimbira za Davide mfumu ya Israeli.
28 Anthu onse anawerama pansi ndi kulambira, pamene oyimba amayimba ndi malipenga. Izi zonse zinapitirira mpaka pa mapeto pa nsembe zopsereza.
29 Zopereka zitatha, mfumu ndi wina aliyense amene anali naye anagwada pansi ndi kulambira.
30 Mfumu Hezekiya ndi akuluakulu ake analamulira Alevi kuti atamande Yehova potsata mawu a Davide ndi mlosi Asafu. Kotero anayimba nyimbo zamatamando mokondwera ndipo anaweramitsa mitu yawo ndi kulambira.
31 Kenaka Hezekiya anati, “Inu mwadzipereka tsopano kwa Yehova. Bwerani ndipo mufike ndi nsembe ndi zopereka zachiyamiko ku Nyumba ya Yehova.” Choncho anthu onse anabweretsa nsembe ndi zopereka zachiyamiko, ndipo anthu onse amene anali ofuna mu mtima mwawo anabweretsa nsembe zopsereza.
32 Chiwerengero cha nsembe zopsereza chimene anthu onse anabweretsa chinali ngʼombe zazimuna makumi asanu ndi awiri, nkhosa zazimuna 100, ana ankhosa aamuna 200 ndipo zonsezi zinali za nsembe yopsereza kwa Yehova.
33 Ziweto zimene zinapatulidwa kukhala nsembe zinalipo ngʼombe zazimuna 600, nkhosa ndi mbuzi 3,000.
34 Koma ansembe anali ochepa kuti asende zonse zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza mpaka ntchito yonse inatha ndipo mpaka ansembe ena atadziyeretsa, pakuti Alevi anachita changu kudziyeretsa kulekana ndi momwe anachitira ansembe.
35 Panali nsembe zopsereza zochuluka, pamodzi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano ndi nsembe yachakumwa imene imachitika pamodzi ndi nsembe yopsereza. Kotero ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu inakhazikitsidwanso.
36 Hezekiya ndi anthu onse anakondwera pa zimene Mulungu anachitira anthu ake, chifukwa zinachita mwamsangamsanga.