< 2 Mbiri 28 >
1 Ahazi anali ndi zaka makumi awiri pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Iye sanachite zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide kholo lake.
viginti annorum erat Achaz cum regnare coepisset et sedecim annis regnavit in Hierusalem non fecit rectum in conspectu Domini sicut David pater eius
2 Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo anawumbanso mafano a chipembedzo cha Abaala.
sed ambulavit in viis regum Israhel insuper et statuas fudit Baalim
3 Iye amapsereza nsembe ku chigwa cha Hinomu, ndipo anaperekanso ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza kutsatira njira zonyansa za mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli.
ipse est qui adolevit incensum in valle Benennon et lustravit filios suos in igne iuxta ritum gentium quas interfecit Dominus in adventu filiorum Israhel
4 Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzerapo mafano, pamwamba pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu.
sacrificabat quoque et thymiama succendebat in excelsis et in collibus et sub omni ligno frondoso
5 Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wake anamupereka mʼmanja mwa mfumu ya Aramu. Aaramu anamugonjetsa ndipo anagwira ukapolo anthu ake ambiri napita nawo ku Damasiko. Yehova anamuperekanso mʼmanja mwa mfumu ya Israeli, imene inamuzunza ndi kumuphera anthu ake ambiri.
tradiditque eum Dominus Deus eius in manu regis Syriae qui percussit eum magnamque praedam de eius cepit imperio et adduxit in Damascum manibus quoque regis Israhel traditus est et percussus plaga grandi
6 Pa tsiku limodzi, Peka mwana wa Remaliya anapha asilikali 120,000 mu Yuda chifukwa Yuda anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo.
occiditque Phacee filius Romeliae de Iuda centum viginti milia in die uno omnes viros bellatores eo quod reliquissent Dominum Deum patrum suorum
7 Zikiri msilikali wa ku Efereimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu woyangʼanira nyumba yaufumu, ndi Elikana wachiwiri kwa mfumu.
eodem tempore occidit Zechri vir potens ex Ephraim Masiam filium regis et Ezricam ducem domus eius Helcanam quoque secundum a rege
8 Aisraeli anagwira ukapolo abale awo, akazi, ana aamuna ndi ana aakazi okwanira 200,000. Iwo anafunkhanso katundu wambiri amene anapita naye ku Samariya.
ceperuntque filii Israhel de fratribus suis ducenta milia mulierum puerorum et puellarum et infinitam praedam pertuleruntque eam in Samariam
9 Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba.
ea tempestate erat ibi propheta Domini nomine Oded qui egressus obviam exercitui venientium in Samariam dixit eis ecce iratus Dominus Deus patrum vestrorum contra Iudam tradidit eos manibus vestris et occidistis illos atrociter ita ut caelum pertingeret vestra crudelitas
10 Ndipo tsopano mukufuna kuti amuna ndi akazi a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akhale akapolo anu.
insuper filios Iuda et Hierusalem vultis vobis subicere in servos et ancillas quod nequaquam facto opus est peccatis enim super hoc Domino Deo vestro
11 Tsono mvereni! Abwezeni abale anu amene mwawagwira ukapolo, pakuti mkwiyo wa Yehova uli pa inu.”
sed audite consilium meum et reducite captivos quos adduxistis de fratribus vestris quia magnus furor Domini inminet vobis
12 Tsono atsogoleri ena a ku Efereimu, Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilayi anatsutsana nawo amene ankachokera ku nkhondo kuja.
steterunt itaque viri de principibus filiorum Ephraim Azarias filius Iohanan Barachias filius Mosollamoth Hiezechias filius Sellum et Amasa filius Adali contra eos qui veniebant de proelio
13 Iwo anati, “Musabweretse akapolowo kuno, pakuti ife tidzakhala olakwa pamaso pa Yehova. Kodi mukufuna kuwonjezera pa machimo athu ndi kulakwa kwathu? Pakuti zolakwa zathu ndi zambiri kale ndipo mkwiyo wake woopsa uli pa Israeli.”
et dixerunt eis non introducetis huc captivos ne peccemus Domino quare vultis adicere super peccata nostra et vetera cumulare delicta grande quippe peccatum est et ira furoris Domini inminet super Israhel
14 Kotero asilikali aja anawasiya akapolowo pamodzi ndi katundu amene analanda ku nkhondo pamaso pa akuluakulu ndi gulu lonse la anthu.
dimiseruntque viri bellatores praedam et universa quae ceperant coram principibus et omni multitudine
15 Anthu amene atchulidwa mayina aja anatenga akapolowo, ndipo kuchokera pa zolanda ku nkhondo, anawaveka onse amene anali maliseche. Anawapatsa zovala ndi nsapato, chakudya ndi chakumwa ndi mankhwala. Onse amene anali ofowoka anawakweza pa abulu. Choncho anabwera nawo kwa abale awo ku Yeriko, Mzinda wa Migwalangwa, ndipo kenaka anawabweza ku Samariya.
steteruntque viri quos supra memoravimus et adprehendentes captivos omnesque qui nudi erant vestierunt de spoliis cumque vestissent eos et calciassent et refecissent cibo ac potu unxissent quoque propter laborem et adhibuissent eis curam quicumque ambulare non poterant et erant inbecillo corpore inposuerunt eos iumentis et adduxerunt Hierichum civitatem Palmarum ad fratres eorum ipsique reversi sunt Samariam
16 Pa nthawi imeneyo mfumu Ahazi inatumiza mawu kwa mfumu ya ku Asiriya kupempha chithandizo.
tempore illo misit rex Achaz ad regem Assyriorum auxilium postulans
17 Ankhondo a ku Edomu anabweranso ndi kuthira nkhondo Yuda ndi kugwira akapolo.
veneruntque Idumei et percusserunt multos ex Iuda et ceperunt praedam magnam
18 Pamenepo nʼkuti Afilisti atathira nkhondo mizinda ya mʼmbali mwa phiri ndi ku Negevi ku Yuda. Iwo analanda mizindayo nakhala ku Beti-Semesi, Ayaloni ndi Gederoti, komanso Soko, Timna ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yawo yozungulira.
Philisthim quoque diffusi sunt per urbes campestres et ad meridiem Iuda ceperuntque Bethsames et Ahilon et Gaderoth Soccho quoque et Thamnam et Gamzo cum viculis suis et habitaverunt in eis
19 Yehova anapeputsa Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi ya Israeli, pakuti analimbikitsa zoyipa ku Yuda ndipo anali munthu wosakhulupirika kwambiri pamaso pa Yehova.
humiliaverat enim Dominus Iudam propter Achaz regem Iuda eo quod nudasset eum auxilio et contemptui habuisset Dominum
20 Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera kwa iye, ndipo anabweretsa mavuto mʼmalo momuthandiza.
adduxitque contra eum Thaglathphalnasar regem Assyriorum qui et adflixit eum et nullo resistente vastavit
21 Ahazi anatenga zinthu zochokera mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba yaufumu ndi kwa atsogoleri ndipo anazipereka kwa mfumu ya ku Asiriya, koma zimenezo sizinamuthandize.
igitur Achaz spoliata domo Domini et domo regum et principum dedit regi Assyriorum munera et tamen nihil ei profuit
22 Pa nthawi yake yamavutoyi mfumu Ahazi inapitirira kukhalabe yosakhulupirika pamaso pa Yehova.
insuper et in tempore angustiae suae auxit contemptum in Dominum ipse per se rex Achaz
23 Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse.
immolavit diis Damasci victimas percussoribus suis et dixit dii regum Syriae auxiliantur eis quos ego placabo hostiis et aderunt mihi cum e contrario ipsi fuerint ruina eius et universo Israhel
24 Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu.
direptis itaque Achaz omnibus vasis domus Dei atque confractis clusit ianuas templi Dei et fecit sibi altaria in universis angulis Hierusalem
25 Mu mzinda uliwonse wa Yuda anamangamo malo achipembedzo, operekerapo nsembe zopsereza kwa milungu ina ndipo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mulungu wa makolo ake.
in omnibus quoque urbibus Iuda extruxit aras ad cremandum tus atque ad iracundiam provocavit Dominum Deum patrum suorum
26 Zochitika zina pa ulamuliro wake ndi machitidwe ake onse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli.
reliqua autem sermonum eius et omnium operum priorum et novissimorum scripta sunt in libro regum Iuda et Israhel
27 Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sanamuyike mʼmanda a mafumu a Israeli. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
dormivitque Achaz cum patribus suis et sepelierunt eum in civitate Hierusalem neque enim receperunt eum in sepulchra regum Israhel regnavitque Ezechias filius eius pro eo