< 2 Mbiri 23 >

1 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaonetsa mphamvu zake. Iye anachita pangano ndi olamulira magulu a anthu 100: Azariya mwana wa Yerohamu, Ismaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.
Mas al séptimo año, Joiada se animó, y tomó consigo en alianza a los centuriones, a Azarías, hijo de Jeroham, y a Ismael, hijo de Johanán, y a Azarías, hijo de Obed, y Masías, hijo de Adaias, y Elisafat, hijo de Zecri:
2 Iwo anayendayenda mʼdziko la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli ochokera mʼmizinda yonse. Atabwera ku Yerusalemu,
Los cuales rodeando por Judá, juntaron los Levitas de todas las ciudades de Judá, y los príncipes de las familias de Israel, y vinieron a Jerusalem.
3 msonkhano wonse unachita pangano ndi mfumu mu Nyumba ya Mulungu. Yehoyada anawawuza kuti, “Mwana wa mfumu adzalamulira monga ananenera Yehova zokhudza ana a Davide.
Y toda la multitud hizo alianza con el rey en la casa de Dios; y él les dijo: He aquí el hijo del rey, el cual reinará, como Jehová lo ha dicho de los hijos de David.
4 Tsopano zimene muti muchite ndi izi: Limodzi mwa magawo atatu a ansembe ndi Alevi amene mudzakhale pa ntchito pa Sabata muzikalondera pa khomo,
Lo que habéis de hacer, es que la tercera parte de vosotros, los que entran el sábado, estarán por porteros con los sacerdotes y los Levitas:
5 ndi limodzi la magawo atatu likakhale ku nyumba yaufumu ndipo limodzi la magawo atatu likakhale ku chipata cha Maziko ndipo anthu ena onse akakhale mʼmabwalo a Nyumba ya Yehova.
Y la otra tercera parte, a la casa del rey: y la otra tercera parte, a la puerta del cimiento: y todo el pueblo estará en los patios de la casa de Jehová.
6 Musalole aliyense kulowa mʼNyumba ya Yehova kupatula ansembe ndi Alevi amene akutumikira. Iwo atha kutero chifukwa apatulidwa koma anthu ena onse ayenera kumvera zimene Yehova walamula.
Y ninguno entre en la casa de Jehová, sino los sacerdotes y los Levitas que sirven: estos entrarán, porque son santos: y todo el pueblo hará la guardia de Jehová.
7 Alevi akhale mozungulira mfumu, munthu aliyense ali ndi chida chake mʼmanja. Aliyense amene alowe mʼNyumba ya Mulungu ayenera kuphedwa. Mukhale nayo pafupi mfumu kulikonse kumene izipita.”
Y los Levitas cercarán al rey de todas partes, y cada uno tendrá sus armas en la mano; y cualquiera que entrare en la casa, muera: y estaréis con el rey cuando entrare, y cuando saliere.
8 Alevi ndi anthu onse a ku Yuda anachita monga momwe wansembe Yehoyada anawalamulira. Aliyense anatenga anthu ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene amapita kukapuma, pakuti wansembe Yehoyada sanalole gulu lililonse kuti lipite.
Y los Levitas y todo Judá lo hicieron todo como lo había mandado el sacerdote Joiada: y tomó cada uno los suyos, los que entraban el sábado, y los que salían el sábado: porque el sacerdote Joiada no dio licencia a las compañías.
9 Ndipo Yehoyada anapereka kwa atsogoleri a magulu a anthu 100 mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazingʼono zimene zinali za Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Mulungu.
Dio también el sacerdote Joiada a los centuriones las lanzas, paveses, y escudos, que habían sido del rey David, que estaban en la casa de Dios.
10 Iye anayika anthu onse, aliyense ali ndi chida mʼdzanja lake mozungulira mfumu pafupi ndi guwa ndi Nyumba ya Mulungu, kuyambira mbali ya kummwera mpaka kumpoto kwa Nyumba ya Mulungu.
Y puso en orden a todo el pueblo, teniendo cada uno su espada en la mano, desde el rincón derecho del templo hasta el izquierdo, al altar y a la casa, en derredor del rey de todas partes.
11 Yehoyada ndi ana ake anatulutsa mwana wa mfumu ndipo anamumveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano namulonga ufumu. Yehoyada ndi ana ake anamudzoza ndipo anafuwula kuti, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”
Entonces sacaron al hijo del rey, y pusiéronle la corona y el testimonio, e hiciéronle rey. Y Joiada y sus hijos le ungieron, diciendo: Viva el rey.
12 Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga ndi kukondwerera mfumu, anapita ku Nyumba ya Yehova komwe kunali anthuko.
Y como Atalía oyó el estruendo del pueblo que corría, y de los que bendecían al rey, vino al pueblo a la casa de Jehová;
13 Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
Y mirando vio al rey que estaba junto a su columna a la entrada, y los príncipes y los trompetas junto al rey, y que todo el pueblo de la tierra hacía alegrías, y sonaban bocinas, y cantaban con instrumentos de música, los que sabían alabar: entonces Atalía rompió sus vestidos, y dijo: Conjuración, conjuración:
14 Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,”
Y sacando el pontífice Joiada los centuriones y capitanes del ejército, díjoles: Sacádla de dentro del cercado: y el que la siguiere, muera a cuchillo: porque el sacerdote había mandado, que no la matasen en la casa de Jehová.
15 choncho anamugwira pamene amafika pa chipata cha Kavalo pa bwalo la nyumba yaufumu, ndipo anamuphera pamenepo.
Y ellos pusieron las manos en ella, y ella se entró en la entrada de la puerta de los caballos de la casa del rey, y allí la mataron,
16 Tsono Yehoyada anachita pangano, iye mwini ndi anthu onse ndiponso mfumu kuti adzakhala anthu a Yehova.
Y Joiada hizo alianza entre sí, y todo el pueblo, y el rey, que serían pueblo de Jehová.
17 Anthu onse anapita ku kachisi wa Baala ndipo anamugwetsa. Iwo anaphwanya maguwa ndi mafano ndi kupha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwawo.
Después de esto entró todo el pueblo en el templo de Baal, y le derribaron, y también sus altares: y quebraron sus imágenes. Y asimismo mataron delante de los altares a Matán sacerdote de Baal.
18 Kenaka Yehoyada anayika ansembe, omwe anali Alevi kukhala oyangʼanira Nyumba ya Yehova, amene Davide anawapatsa ntchito yoti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼNyumba ya Mulungu, monga zinalembedwa mʼmalamulo a Mose kuti azitero akukondwera ndi kuyimba monga Davide analamulira.
Después de esto Joiada ordenó los oficios en la casa de Jehová debajo de la mano de los sacerdotes y de los Levitas, como David los había distribuido en la casa de Jehová, para ofrecer los holocaustos a Jehová, como está escrito en la ley de Moisés, con gozo y cantares, conforme a la ordenación de David.
19 Ndipo anayika alonda a pa khomo pa zipata za Nyumba ya Yehova kuti aliyense amene ndi odetsedwa asalowe.
Puso también porteros a las puertas de la casa de Jehová, para que por ninguna vía entrase ningún inmundo.
20 Iye anatenga olamulira magulu a anthu 100, anthu otchuka, olamulira anthu ndi anthu onse a mʼderalo ndipo anabweretsa mfumu kuchokera ku Nyumba ya Mulungu. Iwo anapita ku nyumba yaufumu kudzera ku Chipata Chakumitu ndipo anayikira mfumu mpando wolemekezeka,
Tomó después a los centuriones, y los principales, y los que gobernaban el pueblo, y a todo el pueblo de la tierra, y llevó al rey de la casa de Jehová: y viniendo hasta el medio de la puerta mayor de la casa del rey, asentaron al rey sobre el trono del reino.
21 ndipo anthu onse a mʼderali anakondwera. Tsono mu mzinda munali bata chifukwa Ataliya anaphedwa ndi lupanga.
Y todo el pueblo de la tierra hizo alegrías, y la ciudad estuvo quieta: y a Atalía mataron a cuchillo.

< 2 Mbiri 23 >