< 1 Timoteyo 3 >

1 Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino.
Ano, je to tak: Být v církvi autoritou, to je velký úkol.
2 Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa.
Takový člověk musí být bezúhonný, věrný své jediné manželce, střídmý, rozvážný, pořádný. Vyžadují se také pohostinnost, pedagogické vlohy, taktnost, smířlivost a nezištnost. Nesmí být pijan ani rváč, rodinu musí mít spořádanou, děti vychované k poslušnosti a poctivosti.
3 Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama.
4 Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni.
5 (Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?)
Jak by mohl prospět církvi ten, kdo by vlastní rodinu dobře vést nedokázal?
6 Asakhale wongotembenuka mtima kumene kuopa kuti angadzitukumule napezeka pa chilango monga Satana.
Ve víře a v církvi nesmí být nováčkem, aby mu pýcha nestoupla do hlavy a nepřivedla ho do pádu.
7 Ayeneranso kukhala munthu wambiri yabwino ndi akunja, kuti anthu asamutonze nagwa mu msampha wa Satana.
I mimo církev musí mít dobrou pověst, aby mu pomluvy nepřekážely v práci.
8 Momwemonso atumiki, akhale anthu oyenera ulemu, woona mtima, osakhala okonda zoledzeretsa, osakonda kupeza zinthu mwachinyengo.
Také správci společného majetku musí mít stejné morální kvality jako pastýři: nesmějí se přetvařovat, holdovat alkoholu ani mamonu.
9 Ayenera kugwiritsa mozama choonadi cha chikhulupiriro ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino.
Bohem svěřenou pravdu ať uchovávají v čistém srdci. Pro tuto službu vybírejte jen muže s bezvadnou pověstí.
10 Ayambe ayesedwa kaye, ndipo ngati palibe kanthu kowatsutsa, aloleni akhale atumiki.
11 Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.
Také ženy musí být rozvážné, diskrétní, spolehlivé a střídmé. Pro tento úřad je rovněž podmínkou manželská věrnost a spořádané rodinné poměry.
12 Mtumiki akhale wokhulupirika kwa mkazi wake ndipo ayenera kukhala wosamalira bwino ana ake ndi onse a pa khomo pake.
13 Iwo amene atumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndipo amakhala chitsimikizo chachikulu cha chikhulupiriro chawo mwa Khristu Yesu.
Všem, kteří konají dobře svou službu, bude odměnou stále rostoucí úcta ostatních i vlastní jistota ve víře v Ježíše Krista.
14 Ngakhale ndili ndi chiyembekezo choti ndifika komweko posachedwapa, ndikukulemberani malangizo awa.
I když doufám, že se brzy uvidíme,
15 Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi.
pro případ většího zdržení ti všechno píšu, abys věděl, jak vybírat pracovníky v církvi živého Boha, která je sloupem a pevností pravdy.
16 Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu: Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu anamuchitira umboni, angelo anamuona, analalikidwa pakati pa mitundu yonse, dziko lapansi linamukhulupirira, anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.
Všichni jsou zajedno v tom, jak jedinečná je pravda, kterou nám Bůh odhalil: Kristus přišel na svět v lidském těle, veden Božím Duchem, zvítězil nad hříchem, jako vítěz představen v nebesích, zvěstován všem národům, vírou uznán ve světě, korunován věčnou slávou.

< 1 Timoteyo 3 >